iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa padziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu.
Genesis 7:15 - Buku Lopatulika Ndipo zinalowa kwa Nowa m'chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zinalowa kwa Nowa m'chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nowa adaloŵa m'chombomo pamodzi ndi zamoyo zonse zazimuna ndi zazikazi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nowa analowa mu chombo muja pamodzi ndi zamoyo zonse. |
iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa padziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu.
Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.
zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.