Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.
Genesis 6:22 - Buku Lopatulika Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nowa anachita zonse monga Mulungu anamulamulira. |
Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.
Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.
zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose.
nalowa nalo likasa mu chihema, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.
pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.