Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.
Genesis 6:14 - Buku Lopatulika Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m'chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m'chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Udzipangire chombo ndipo uchipange ndi matabwa a mtengo wa mnjale. Upange zipinda m'menemo, ndipo uchimate phula kunja kwake ndi m'kati momwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. |
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.
Kupanga kwake ndi kotere: m'litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwake mikono makumi asanu, m'msinkhu mwake mikono makumi atatu.
Koma pamene sanathe kum'bisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa mtsinje.
Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa,
Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo.
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;