Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m'dziko la Ejipito,
Genesis 50:8 - Buku Lopatulika ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapitanso ndi onse a banja lake, abale ake, ndi onse a banja la bambo wake. Ku Goseni kuja kudangotsala ana okhaokha, nkhosa zao, abusa ndi ng'ombe zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni |
Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m'dziko la Ejipito,
Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.