Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.
Genesis 50:6 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adamuyankha kuti, “Pita ukaike atate ako monga momwe adakulumbiritsira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.” |
Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.
Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.
Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m'dziko la Ejipito,