Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.
Genesis 50:26 - Buku Lopatulika Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi mu Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi m'Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Yosefe adamwalira ali wa zaka 110. Mtembo wake adaukonza ndi mankhwala, naukhazika m'bokosi ku Ejipito komweko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto. |
Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.
Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Ndipo Yosefe anakhala mu Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi.
Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi.