Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.
Genesis 50:23 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakhala moyo mpaka kuwona adzukulu ake, ana a Efuremu. Pamene ana a Makiri mwana wa Manase adabadwa, Yosefe adaŵalandira m'banja mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake. |
Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.
Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.
Ndipo Yosefe anakhala mu Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi.
Ana a Manase ndiwo Asiriele amene mkazi wake anambala. Koma mkazi wake wamng'ono Mwaramu anabala Makiri atate wa Giliyadi;
Ndipo zitatha izi, Yobu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi mphambu makumi anai, naona ana ake ndi zidzukulu zake mibadwo inai.
Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi hafu la fuko la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi mizinda yake m'malire mwao, ndiyo mizinda ya dziko lozungulirako.
Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase ananka ku Giliyadi, naulanda, napirikitsa Aamori anali m'mwemo.
Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.