Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.
Genesis 50:17 - Buku Lopatulika Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ‘Ndikumpempha Yosefe kuti akhululukire cholakwa cha abale ake chimene adamchitira.’ Pepani tsopano tikhululukireni cholakwa chimene ife, akapolo a Mulungu wa atate anu, tidachita.” Atangomva zimenezi Yosefe adayambapo kulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira. |
Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.
Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito.
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.
Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.
Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.
Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.
Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.