Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
Genesis 50:12 - Buku Lopatulika Ndipo ana ake aamuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana ake amuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Yakobe adachitadi monga momwe bambo wao adaaŵalamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: |
Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.