Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Genesis 5:27 - Buku Lopatulika masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamwalira ali wa zaka 969. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira. |
Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameki, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana aamuna ndi aakazi:
Ndipo Lameki anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;
Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.
Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka chakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.
Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.