masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.
Genesis 5:21 - Buku Lopatulika Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Enoki ali wa zaka 65, adabereka mwana dzina lake Metusela. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. |
masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.
ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani,
Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeke, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;
Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi,