Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 49:7 - Buku Lopatulika

Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa mu Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa m'Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo m'Israele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Matemberero aŵagwere, chifukwa mkwiyo wao ndi woopsa kwambiri, ukali wao utembereredwenso, chifukwa imeneyo ndi nkhalwe. Ndidzaŵamwaza iwowo m'dziko lonse la Yakobe. Ndidzaŵabalalitsa pakati pa Israele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi ndi ukali wawo wankhanza choterewu! Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.

Onani mutuwo



Genesis 49:7
11 Mawu Ofanana  

Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.


Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la ana a Benjamini, mizinda iyi yotchulidwa maina ao.


Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.


Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa.


Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.