Genesis 49:5 - Buku Lopatulika Simeoni ndi Levi ndiwo abale; zida za mphulupulu ndizo malupanga ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Simeoni ndi Levi ndiwo abale; zida za mphulupulu ndizo malupanga ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Simeoni ndi Levi mpachibale pao, amagwiritsa ntchito zida zankhondo pochita chiwawa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo, anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano. |
Ndi kumalire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.
Motero ana a Israele anapatsa Alevi mizinda iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.
Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.