Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 49:21 - Buku Lopatulika

Nafutali ndi mbawala yomasuka; apatsa mau abwino.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nafutali ndi mbawala yomasuka; apatsa mau abwino.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Nafutali ali ngati insa yongoyenda mwaufulu, imene imabala ana okongola.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Nafutali ali ngati mbawala yayikazi yokhala ndi ana okongola kwambiri.

Onani mutuwo



Genesis 49:21
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali.


Ndi ana aamuna a Nafutali: Yazeele, ndi Guni, ndi Yezere ndi Silemu.


Ndipo ananena naye, kuti, Mukawachitira chokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha.


Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.


Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala zakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.


Inde, mbawalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ake, chifukwa mulibe udzu.


Za Nafutali anati, Nafutali, wokhuta nazo zomkondweretsa, wodzala ndi mdalitso wa Yehova; landira kumadzulo ndi kumwera.


Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.


Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?


Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa, Nafutali yemwe poponyana pamisanje.