Genesis 49:19 - Buku Lopatulika Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye; koma iye adzapsinja pa chitendeni chao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye; koma iye adzapsinja pa chitende chao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Gadi anthu achifwamba adzamthira nkhondo, koma iyeyo adzaŵatembenukira nkuŵapirikitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo, koma iye adzawathamangitsa. |
Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.
Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.
Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;