Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.
Genesis 49:16 - Buku Lopatulika Dani adzaweruza anthu ake, monga limodzi la mafuko a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dani adzaweruza anthu ake, monga limodzi la mafuko a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Dani adzalamulira anthu ake. Anthuwo adzalingana ndi mafuko ena a Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli. |
Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.
Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.
Dani adzakhala njoka m'khwalala, songo panjira, imene iluma zitendene za kavalo, kuti womkwera wake agwe chambuyo.
Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.