Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara.
Genesis 49:14 - Buku Lopatulika Isakara ndiye bulu wolimba, alinkugona pakati pa makola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Isakara ndiye bulu wolimba, alinkugona pakati pa makola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Isakara ali ngati bulu wamphamvu, amagona chotambasuka pakati pa makola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Isakara ali ngati bulu wamphamvu wogona pansi pakati pa makola. |
Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara.
Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.
Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.
Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.
Ndi za Zebuloni anati, Kondwera, Zebuloni, ndi kutuluka kwako; ndi Isakara, m'mahema mwako.
Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye mu Samiri ku mapiri a Efuremu.