Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 48:6 - Buku Lopatulika

Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m'cholowa chao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m'cholowa chao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma obadwa pambuyo pa iwowo, ndi ako amenewo. Adzalandira choloŵa chao pamodzi ndi achibale ao.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma amene ati adzabadwe pambuyo pa iwowa adzakhala ako ndipo cholowa chawo chidzadziwika ndi mayina a abale awo.

Onani mutuwo



Genesis 48:6
3 Mawu Ofanana  

Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma mizinda yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.