Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
Genesis 48:20 - Buku Lopatulika Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero adaŵadalitsa pa tsiku limenelo ndi mau akuti, “Aisraele adzatchula maina anu podalitsa. Adzanena kuti, ‘Mulungu akudalitseni inu monga Efuremu ndi Manase.’ ” Mwa njira imeneyi adaika Efuremu patsogolo pa Manase. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati, “Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati: Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.” Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase. |
Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:
Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.
Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
Ndi chikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pamutu wa ndodo yake.
Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?