Genesis 48:17 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pamutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pamutu wa Efuremu ndi kuliika pamutu wa Manase. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pa mutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pa mutu wa Efuremu ndi kuliika pa mutu wa Manase. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe ataona kuti bambo wake wasanjika dzanja lamanja pamutu pa Efuremu, adakhumudwa. Motero adatenga dzanja la bambo wake kulichotsa pamutu pa Efuremu, nalisanjika pamutu pa Manase. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase, |
Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.
Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.
pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,
Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.