Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.
Genesis 47:8 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Farao adafunsa Yakobe kuti, “Muli ndi zaka zingati?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatero, Farao anafunsa Yakobo kuti, “Muli ndi zaka zingati?” |
Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.
Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wake, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao.
Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu?