Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'mizinda; chakudya cha m'minda, yozinga mizinda yonse, anachisunga m'menemo.
Genesis 47:21 - Buku Lopatulika Tsono anthu, anasunthira iwo kumizinda kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono anthu, anasunthira iwo kumidzi kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe adaŵasandutsa akapolo anthuwo ponseponse m'dziko la Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo Yosefe anawasandutsa anthu onse kukhala akapolo a Farao, kuchokera ku malire a mbali ina ya Igupto kukafika ku malire a mbali ina ya dzikolo. |
Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'mizinda; chakudya cha m'minda, yozinga mizinda yonse, anachisunga m'menemo.
Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.
Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitse dziko lao.