tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.
Genesis 47:20 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yosefe adagulira Farao dziko lonse la Ejipito. Mwejipito aliyense adagulitsa minda yake chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri. Motero dziko lonse lidasanduka la Farao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yosefe anamugulira Farao dziko lonse la Igupto. Aliyense mu Igupto anagulitsa munda wake chifukwa njala inakula kwambiri. Dziko lonse linasanduka la Farao, |
tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.
Tsono anthu, anasunthira iwo kumizinda kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake.