Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Genesis 47:15 - Buku Lopatulika Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndalama zonse zitaŵathera anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani, Aejipito ambiri adabwera kwa Yosefe, namuuza kuti, “Tipatseniko chakudya! Musatilekerere kuti tife, chitanipo kanthu! Ndalama zathu zonse zatha!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a ku Igupto ndi Kanaani ndalama zitawathera, Aigupto onse anabwera kwa Yosefe nati, “Tipatseni chakudya. Nanga tiferenji pamaso panu? Ndalama zathu zatha.” |
Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng'ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng'ombe zanu ngati ndalama zatsirizika.
Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani.
Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.
Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho.
Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; chifukwa chake muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tilikufika tsiku labwino; mupatse chilichonse muli nacho m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.