Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.
Genesis 47:14 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe adasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a ku Ejipito pamodzi ndi a ku Kanani adaamwaza pogula tirigu. Ndalama zonsezo adazitenga napita nazo kunyumba kwa Farao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a mu Igupto ndi Kanaani ankapereka pogula tirigu, ndipo anabwera nazo ku nyumba kwa Farao. |
Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.
Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.
Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;