Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Genesis 47:13 - Buku Lopatulika Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani tinalefuka chifukwa cha njalayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Njala ija idakula kwambiri, kotero kuti panalibe chakudya pa dziko lonse lapansi, ndipo anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani komwe adafooka nayo njalayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Njala inakula kwambiri motero kuti chakudya chinasowa mʼdziko lonse. Anthu a ku Igupto ndi ku Kanaani analefuka nayo njalayo. |
Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.
Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupserera monga chipululu, kuti anthu asapitemo?
Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.
Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani yense, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeze chakudya makolo athu.