Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.
Genesis 46:9 - Buku Lopatulika Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ana amuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndi ana aŵa a Rubeni: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aamuna a Rubeni ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. |
Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.
Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.
Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.
Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.
Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.