Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Genesis 46:5 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana aamuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao aang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yakobe adanyamuka kuchoka ku Beereseba. Ana ake a Israele aja adakweza bambo wao Yakobe, pamodzi ndi akazi ndi ana, pa ngolo zimene Farao adaatumiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo. |
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.
Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.
Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;
Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu aang'ononso.
Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.
Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu mu Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano.