Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;
Genesis 45:25 - Buku Lopatulika Ndipo anakwera kutuluka mu Ejipito, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakwera kutuluka m'Ejipito, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono iwo adachoka ku Ejipito, kubwerera ku Kanani kwa bambo wao Yakobe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anachoka ku Igupto nafika kwa abambo awo Yakobo mʼdziko la Kanaani. |
Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;
Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.