Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Genesis 45:23 - Buku Lopatulika Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za mu Ejipito, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za m'Ejipito, ndi abulu akazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bambo wake adamtumizira abulu khumi osenza zipatso zokoma za ku Ejipito, ndi abulu khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za bambo wake zapaulendo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo abambo ake anawatumizira izi: abulu khumi osenza zinthu zabwino kwambiri za ku Igupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za pa ulendo wake. |
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;
Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.
nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.