Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 45:22 - Buku Lopatulika

Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adapatsanso aliyense zovala zachikondwerero, koma Benjamini adampatsa mashikeli asiliva okwana 300, ndi zovala zisanu zachikondwerero.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anaperekanso kwa aliyense zovala zatsopano, koma kwa Benjamini anapereka siliva wolemera pafupifupi makilogalamu anayi ndi zovala zisanu.

Onani mutuwo



Genesis 45:22
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.


Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za mu Ejipito, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira.


Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.


Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.


Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu;


Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.