Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 45:19 - Buku Lopatulika

Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Uŵauze kuti atenge ngolo za kuno ku Ejipito, kuti akazi ao akakwerepo pamodzi ndi ana omwe. Ndithu akamtenge bambo wao akabwere kuno.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Uwawuzenso kuti, ‘Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno.

Onani mutuwo



Genesis 45:19
8 Mawu Ofanana  

Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Ejipito ndi zanu.


Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.


Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;


Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana aamuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao aang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye.


Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga awiru anapereka galeta ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa chihema.