Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.
Genesis 45:17 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Farao adauza Yosefe kuti, “Uŵauze abale ako kuti asenzetse nyama zao katundu, ndipo abwerere ku Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anati kwa Yosefe, “Uwawuze abale ako kuti, ‘Senzetsani nyama zanu katundu ndi kubwerera ku dziko la Kanaani. |
Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.
katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.