Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake.
Genesis 45:16 - Buku Lopatulika Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zitamveka kunyumba kwa Farao kuti abale a Yosefe abwera, Faraoyo ndi antchito ake onse adakondwa kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akunyumba kwa Farao atamva kuti abale ake a Yosefe abwera, Farao pamodzi ndi nduna zake zonse anakondwera. |
Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake.
Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.
Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Ejipito.
Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;
Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.
ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti. Ndipo chinthuchi chinamkonda mfumu, nachita chomwecho.
Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.
Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:
Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.
amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.