Genesis 45:14 - Buku Lopatulika Ndipo anagwa pakhosi pake pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anagwa pakhosi pake pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero adakumbatira Benjamini, mng'ono wake uja, nayambanso kulira. Benjamini nayenso adayamba kulira atangomkumbatira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yosefe anakhumbatira Benjamini, mngʼono wake uja nayamba kulira. Nayenso Benjamini anayamba kulira atamukumbatira. |
Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.
Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.
Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.
Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.
Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.