Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu.
Genesis 45:13 - Buku Lopatulika Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse mu Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muuzeni bambo wanga kuti ndili pa ulemerero waukulu ku Ejipito kuno. Mukamuuzenso bambo wanga zonse zimene mwaonazi ndipo fulumirani, mubwere naye kuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukawawuze abambo anga kuti ndili pa ulemerero ku dziko la Igupto kuno ndi zonse zimene mwaziona. Tsopano fulumirani kuti mukabwere nawo kuno abambo anga.” |
Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu.
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.
Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.