Genesis 45:12 - Buku Lopatulika Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono nonsenu ndi Benjamini, mng'ono wangayu, mungathe kuwona kuti ndinedi amene ndikulankhula nanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsono inu nonse pamodzi ndi mʼbale wangayu Benjamini, mukuona kuti ndi inedi amene ndikuyankhula nanu. |
ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.
Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse mu Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.
Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndili nazo Ine.
Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.