Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.
Genesis 44:9 - Buku Lopatulika Iye wa akapolo anu ampeza nacho afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye wa akapolo anu ampeza nacho afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono bwana, wina mwa ife akapezeka ndi chikho chimenechi, ndithu aphedwe, ndipo tonsefe tidzakhala akapolo anu, bwana!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati wantchito wanu wina pano atapezeka nacho chikhocho, ameneyo aphedwe ndipo ena tonsefe tidzakhala akapolo anu, mbuye wathu.” |
Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.
Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu.
Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa.
Ndipo Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? Kodi tidzanenanji? Kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tili akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m'dzanja lake.
Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.