Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero.
Genesis 44:6 - Buku Lopatulika Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wantchito uja ataŵapeza, adanena mau omwe adaamuuza aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wantchito uja atawapeza ananena mawu anawuzidwa aja. |
Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero.
Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu achite chotero?
Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.