Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe.
Genesis 44:5 - Buku Lopatulika Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwaberanji chikho chimene mbuyanga amamwera? Amati akafuna kudziŵa zam'tsogolo, amagwiritsa ntchito chikho chimenechi. Ndithu zimene mwachitazi nzoipa kwambiri.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwaberanji chikho chimene mbuye wanga amamweramo ndi kugwiritsa ntchito akafuna kuwombeza? Chimene mwachitachi ndi chinthu choyipa.’ ” |
Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe.
Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ichi nchiyani mwachichita? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu?
Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'galeta mwake.
Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.