Genesis 44:4 - Buku Lopatulika Atatuluka m'mzinda asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atatuluka m'mudzi asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atangoyenda pang'ono kuchoka mumzindamo, Yosefe adauza wantchito wake wamkulu uja kuti, “Nyamuka, uthamangire anthu aja. Ukaŵapeza, uŵafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoipa kwa zabwino? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino? |
tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?
Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.