Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.
Genesis 44:11 - Buku Lopatulika Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero onsewo adatsitsa msanga matumba ao, aliyense nkumasula thumba lake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono onse anafulumira kutsitsa pansi aliyense thumba lake ndi kulitsekula. |
Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.
Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa.
Ndipo iye anafunafuna kuyambira pa wamkulu naleka pa wamng'ono nachipeza chikho m'thumba la Benjamini: