Genesis 44:10 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo wantchitoyo adati, “Chabwino. Komatu wina pakati panupa akapezeka ndi chikhocho, ameneyo akhala kapolo wanga, ena nonsenu muzipita mwaufulu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.” |
Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.
Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ake.
Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake.