Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.
Genesis 43:6 - Buku Lopatulika Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Israele adati, “Chifukwa chiyani mudathinitsa zinthu pa ine pomuuza kuti muli ndi mbale wanu winanso?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Israeli anafunsa kuti, “Bwanji inu munandiputira mavuto oterewa pomuwuza munthuyo kuti muli ndi mʼbale wanu wina?” |
Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.
Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?
Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?