Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.
Genesis 43:4 - Buku Lopatulika Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mukatilola kuti timtenge, tipita kukakugulirani chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukalola kuti mngʼono wathuyu apite nafe, ndiye ife tidzapita kukakugulirani chakudya. |
Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.
Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono.
Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.
Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.