Genesis 43:34 - Buku Lopatulika Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chakudya chomwe ankadyacho chinkachokera patebulo pa Yosefe, koma chakudya chopatsa Benjamini chinkaposa cha onsewo kasanu. Motero onsewo adadya ndi kumwa pamodzi ndi Yosefe mpaka kukhuta, ndipo adasangalala pamodzi naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono ankawagawira chakudya kuchokera pa tebulo la Yosefe. Koma chakudya cha Benjamini chinkaposa cha ena onsewa kasanu. Motero anadya ndi kumwa mpaka kukhuta, ndipo anasangalala pamodzi ndi Yosefe. |
Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.
Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.
Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.
Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.
Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.
Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.
Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.
nanena naye, Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.
koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake.