Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.
Genesis 43:22 - Buku Lopatulika Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo tabwera nazonso ndalama zina zodzagulira chakudya china. Amene adaika ndalama m'matumba mwathu, sitikumudziŵa ai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tabweretsanso ndalama zina kuti tigule chakudya. Sitikudziwa kuti kaya ndani anayika ndalamazo mʼmatumba athu.” |
Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.
nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;
ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.
Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni.