Genesis 43:20 - Buku Lopatulika Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa namuuza kuti, “Pepani bwana, ife tidaabweranso kuno kale kudzagula chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pepani mbuye wathu, ife tinabweranso ulendo woyamba kudzagula chakudya |
Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.
Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.
Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,
ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.
Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?
Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo.