Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.
Genesis 43:13 - Buku Lopatulika mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtengeni mbale wanuyu, ndipo nyamukani, mupitenso kwa munthuyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mutengeninso mngʼono wanuyu ndi kubwerera kwa munthuyo msanga. |
Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.
nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;
Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.