Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda.
Genesis 43:10 - Buku Lopatulika pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikadapanda kuzengereza, tikadapita ndi kubwerako kaŵiri konse tsopano.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmene zililimu, tikanapanda kuchedwa, bwenzi titapita ndi kubwerako kawiri.” |
Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda.
Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;
Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse: